Adziwe mfumu kuti ife tinamuka ku dziko la Yuda, ku nyumba ya Mulungu wamkuru, yomangidwa ndi miyala yaikuru, niikidwa mitengo pamakoma, nicitika mofulumira nchitoyi, nikula m'dzanja mwao.