Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.