1. Ana a deralo, amene anakwera kuturuka m'ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babulo adawatenga ndende kumka nao ku Babulo, nabwerera kumka ku Yerusalemu ndi Yuda, yense ku mudzi wace, ndi awa:
2. ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Moredekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israyeli ndiko:
3. ana a Parosi, zikwi ziwiri ndi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.
4. Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.
5. Ana a Ara, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu.