Ndipo mfumu inati kwa Estere pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nciani? lidzaperekedwa kwa inu; mufunanji? cidzacitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo.