Koma anaciyesa copepuka kumthira manja Moredekai yekha; pakuti adamfotokozera mtundu wace wa Moredekai; potero Hamani anafuna kuononga Ayuda lonse okhala m'ufumu wonse wa Ahaswero, ndiwo a mtundu wa Moredekai.