Koma Vasiti mkazi wamkuruyo anakana kudza pa mau a mfumu adamuuza adindowo; potero mfumu idapsa mtima ndithu, ndi mkwiyo wace unatentha m'kati mwace.