Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israyeli, ndi za Farao mfumu ya Aigupto, kuti aturutse ana a Israyeli m'dziko la Aigupto.