Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona comwe ndidzacitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lace.