Ndipo anaomba capacifuwa, nchito ya mmisiri, monga maombedwe ace a efodi; ca golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.