10. Ndipo abwere yense wa mtima waluso mwa inu, napange zonse zimene Yehova anauza;
11. kacisi, hema wace, ndi cophimba cace, zokowera zace, ndi matabwa ace, mitanda yace, mizati, nsanamira, ndi nsici zace, ndi makamwa ao;
12. likasa, ndi mphiko zace, cotetezerapo, ndi nsaru yocinga yotseka;
13. gome, ndi mphiko zace, ndi zipangizo zace zonse, ndi mkate woonekera;
14. ndi coikapo nyali ca kuunika, ndi zipangizo zace, ndi nyali zace, ndi mafuta a kuunika;
15. ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi mphiko zace, ndi mafuta odzoza, ndi cofukiza ca pfungo lokoma, ndi nsaru yotsekera pakhomo, pa khomo la kacisi;
16. guwa la nsembe yopereza, ndi made amkuwa, mphiko zace, ndi zipangizo zace zonse, mkhate ndi tsinde lace;