Ndipo azibvale Aroni, ndi ana ace, pakulowa iwo ku cihema cokomanako, kapena poyandikiza iwo ku guwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zace pambuyo pace.