Ndipo uzicinga nsaru yocinga pa zokowerazo, nulowetse likasa la mboni kukati kwa nsaru yocinga; ndipo nsaru yocingayo idzakugawirani pakati pa malo opatulika ndi malo opatulikitsa.