27. popeza copfunda cace ndi ici cokha, ndico cobvala ca pathupi pace; azipfundira ciani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandipfuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wacisomo.
28. Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkuru wa anthu a mtundu wako.
29. Usacedwa kuperekako zipatso zako zocuruka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako amuna undipatse Ine.
30. Uzitero nazo ng'ombe zako, ndi nkhosa zako; masiku asanu ndi atatu akhale ndi amai wace; tsiku lacisanu ndi citatu uzimpereka kwa Ine.
31. Ndipo muzindikhalira Ine anthu opatulika; cifukwa cace musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agaru.