19. Ali yense agona ndi coweta aphedwe ndithu.
20. Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, aonongeke konse.
21. Ndipo usasautsa mlendo kapena kumpsinja; pakuti munali alendo m'dziko la Aigupto.
22. Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye ali yense.
23. Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang'ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwao;
24. ndi mkwiyo wanga idzayaka, ndipo ndidzapha inu ndi lupanga; ndipo akazi anu adzakhala amasiye, ndi ana anu omwe.
25. Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamwerengera phindu.
26. Ukati ulandire cikole kaya cobvala ca mnansi wako, koma polowa dzuwa ucibwezere kwa iye;