Ndipo wansembe wa Midyani anali nao ana akazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimweco kuti amwetse gulu la atate wao.