Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wace. Ndipo anamucha dzina lace Mose, nati, Cifukwa ndinambvuula m'madzi.