6. Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu,Dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani.
7. Ndipo ndi ukulu wanu waukuru mwapasula akuukira Inu;Mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati ciputu.
8. Ndipondi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika,Mayendedwe ace anakhala ciriri ngati mulu;Zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.
9. Mdani anati,Ndiwalondola, ndiwakumika, ndidzagawa zofunkha;Ndidzakhuta nao mtima;Ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga.
10. Munaombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza;Anamira m'madzi akuru ngati mtobvu.
11. Manana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova?Manana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera,Woopsa pomyamika, wakucita zozizwa?
12. Mwatambasula dzanja lanu lamanja,Nthaka inawameza,