Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolera njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati. Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kumka ku Aigupto.