1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'dziko la Aigupto, ndi kuti,
2. Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa caka.
3. Mulankhule ndi msonkhano wonse wa Israyeli ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwana wa nkhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwana wa nkhosa pabanja.
4. Banja likaperewera mwana wa nkhosa, munthu ndi mnzace ali pafupi pa nyumba yace atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwana wa nkhosa monga mwa kudya kwao.