Ndipo anyamata ace a Farao ananena naye, Ameneyo amaticitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Aigupto laonongeka?