26. Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; cosatsala ciboda cimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.
27. Koma Yehova analimbitsa mtima wace wa Farao, ndipo anakana kuwaleka amuke.
28. Ndipo Farao ananena naye, Coka pano, uzicenjera usaonenso nkhope yanga; pakuti tsiku limene uonanso nkhope yanga udzafa.
29. Ndipo Mose anati, Mwanena bwino; sindidzaonanso nkhope yanu.