Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ace; ndi ana a Israyeli anamvera iye, nacita monga Yehova adauza Mose.