11. Ndipo Mose anauza anthu tsiku lomwelo, ndi kuti,
12. Aimirire awa pa phiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordano: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini.
13. Naimirire awa pa phiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Aseri, ndi Zebuloni, Dani, ndi Nafitali.
14. Ndipo ayankhe Alevi ndi kunena kwa amuna onse a Israyeli, ndi mau omveka.
15. Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, nchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse: ayankhe ndi kuti, Amen.
16. Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wace kapena mai wace. Ndi anthu onse anene, Amen.
17. Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wace. Ndi anthu onse anene, Amen.
18. Wotembereredwa wakusokeretsa wakhungu m'njira, Ndi anthu onse anene, Amen.