Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye M-aramu wakuti atayike, natsika kumka ku Aigupto, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukuru, wamphamvu, ndi wocuruka anthu ace;