nati nao, Tamverani, Israyeli, muyandikiza kunkhondo lero paadani anu; musalumuka mitima yanu; musacita mantha, kapena kunjenjemera, kapena kuopsedwa pamaso pao;