Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zace, mwina dongo la woumba, mwina citsulo; ufumuwo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya citsulo; popeza mudaona citsulo cosanganizika ndi dongo.