Ndipo anaika Abineri ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ace nilira ku manda a Abineri, nalira anthu onse.