Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka cifukwa ca dziko, ndi mliri wa pa Israyeli unalekeka.