Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwoo Davide nati kwa Yehova, Ndinacimwa kwakukuru ndi cinthu cimene ndinacita; koma tsopano Yehova mucotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinacita kopusa ndithu.