Ndipo Abisai, mbale wa Yoabu, mwana wa Zeruya, anali wamkuru wa atatuwa. Iye natukula mkondo wace pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.