Ndipo Agibeoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golidi wa Sauli kapena nyumba yace; ndiponso sitifuna kupha munthu ali yense wa m'Israyeli. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakucitirani.