Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfliistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzaturuka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israyeli.