Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Sauli ndi mafupa a Jonatani mwana wace kwa anthu a ku Jabezi Gileadi amene anawaba m'khwalala la Betisani, kumene Afilisti adawapacika, tsiku lija Afilistiwo anapha Sauli ku Giliboa;