Abisalomu anatinso, Mwenzi atandiika ine ndikhale woweruza m'dzikomo, kuti munthu yense amene ali ndi mrandu wace kapena cifukwa cace, akadafika kwa ine; ndipo ndikadamcitira zacilungamo!