Ndipo Yoabu anatumiza ku Tekowa, natenga kumeneko mkazi wanzeru, nanena naye, Ukokomezeke monga mfedwa, nubvale zobvala za pamaliro, osadzola mafuta, koma ukhale ngati munthu wamkazi wakulira akufa nthawi yaikuru.