Comweco Amnoni anagona, nadzikokomeza alikudwala; ndipo pamene mfumu inadza kumuona, Amnoni anati kwa mfumuyo, Mulole Tamara mlongo wanga abwere ndi kundipangira timitanda tiwiri pamaso panga, kuti ndikadye ca m'manja mwace.