Ndipo Abisalomu anakamulira anyamata ace, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Amnoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Amnoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, citani camuna.