Ndipo Solomo anali nazo zipinda zikwi zinai za akavalo ndi magareta, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'toidzi ya magareta, ndi m'Yerusalemu kwa mfumu.