Anapanganso magome khumi, nawaika m'Kacisi, asanu ku dzanja lamanja, ndi asanu ku dzanja lamanzere. Napanga mbale zowazira zana limodzi zagolidi.