Macitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonyansa zace anazicita, ndi zija zidapezeka zomtsutsa; taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda; ndi Yehoyakini mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.