Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Akasidi, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osacitira cifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lace.