Koma Neko anatuma mithenga kwa iye, ndi kuti, Ndiri ndi ciani ndi inu, mfumu ya Yuda? sindinafika kuyambana ndi inu lero, koma ndi nyumba imene ndiri nayo nkhondo; ndipo Mulungu anati ndifulumire; lekani kubvutana ndi Mulungu amene ali nane, Iye angakuonongeni.