Namuka Hilikiya ndi iwo aja adawauza mfumu kwa Hulida mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasire wosunga zobvala, amene anakhala m'Yerusalemu m'dera laciwiri, nanena naye mwakuti.