pamodzi ndi iwo oyesedwa mwa cibadwidwe ca amuna, kuyambira a zaka zitatu ndi mphambu, kwa ali yense amene adalowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa nchito yace pa tsiku lace, kukacita za utumiki wao m'udikiro wao monga mwa zigawo zao;