Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza cifundo pamaso pa iwo anawatenga ndende, nadzalowanso m'dziko muno; pakuti Yehova Mulungu wanu ngwa cisomo ndi cifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye,