Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israyeli ndi Yuda onse, nalembanso akalata kwa Efraimu ndi Manase, kuti abwere ku nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, kucitira Yehova Mulungu wa Israyeli Paskha.