Ndi likole linali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwace monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace zana limodzi mphambu makumr awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golidi woona.