Ndi mapiko a akerubi m'litali mwace ndimo mikono makumi awiri; phiko la kerubi mmodzi mikono isanu, lojima khoma la nyumba; ndi phiko linzace mikono isanu, lokhudzana nalo phiko la kerubi wina.