Pamenepo Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, m'phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wace, pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi.