Uziya anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu ziwiri; ndi dzina la mace ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.